Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 25:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chaka chachisanu ndi chiŵiri chopumulacho chidzakupatsani chakudya chokwanira nonsenu, inuyo ndi akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito anu pamodzi ndi alendo amene akukhala nanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Chaka chimene nthakayo ipumula mudzakhala ndi chakudya chokwanira inuyo, akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito ndi alendo okhala nanu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 25:6
9 Mawu Ofanana  

Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.


koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.


Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;


pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.


Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.


ndi ng'ombe zako, ndi nyama zili m'dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao.


Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana.


Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananene mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa