Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 25:5 - Buku Lopatulika

5 Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Musakolole zimene zidamera zokha m'munda mwanu, ndipo musathyole mphesa za mitengo yanu yosathenera. Chaka chimenechi chikhale chopumuza nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Musakolole zimene zinamera zokha mʼmunda mwanu. Musakakolole kapena kuthyola mphesa za mʼmitengo imene simunasadze. Chaka chimenechi nʼchoti nthaka ipumule.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 25:5
5 Mawu Ofanana  

Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.


Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yampesa ndi kudya chipatso chake.


Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m'mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.


koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako.


Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa