Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 24:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chakudyacho chikhale cha Aroni ndi ana ake, ndipo achidyere m'malo oyera, pakuti kwa iyeyo chimenecho nchopatulika kopambana, chochokera pa nsembe yopsereza kwa Chauta. Lamuloli ndi lamuyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 24:9
17 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;


Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova?


Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele, atate wake ndiye Mwejipito, anatuluka mwa ana a Israele; ndi mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraeleyo analimbana naye munthu Mwisraele kuchigono;


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.


Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.


Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.


nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.


Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.


Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?


kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?


Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa