Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 24:4 - Buku Lopatulika

4 Akonze nyalizo pa choikaponyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Akonze nyalizo pa choikapo nyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Aroni ayatse nyale zimene zili pa choikapo chake cha golide wabwino kwambiri, kuti zikhale zoyaka nthaŵi zonse pamaso pa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Aaroni ayatse nyale zimene zili pa choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri kuti zikhale zoyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 24:4
19 Mawu Ofanana  

ndi zoikaponyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide;


mwa kulemera kwakenso cha zoikaponyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikaponyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikaponyali chilichonse;


Anatsekanso pa khomo chipinda cholowera, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.


ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikaponyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo;


choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;


Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikaponyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa.


Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m'chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikaponyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake.


Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.


Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa