Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 23:8 - Buku Lopatulika

8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zotopetsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 23:8
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.


Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova;


Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo.


Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena;


Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.


Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.


Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa