Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 22:3 - Buku Lopatulika

3 Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Munthu wina aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, akayandikira zopatulika zimene Aisraele adazipereka kwa Chauta, pamene iyeyo ali woipitsidwa, asaonekenso pamaso panga. Ine ndine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golide, ndizo chopereka chaufulu cha kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Nena ndi Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.


Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa