Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 22:23 - Buku Lopatulika

23 Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Mungathe kupereka ng'ombe yamphongo kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi, kuti ikhale nsembe yaufulu, koma ikakhala nsembe yolumbirira, singathe kulandiridwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:23
7 Mawu Ofanana  

Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.


Pakuti munthu aliyense wokhala nacho chilema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mphuno, kapena wamkulu chiwalo,


Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto paguwa la nsembe.


Nyama yofula, kapena chophwanya kapena chosansantha, kapena chotudzula, kapena chodula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamachita ichi m'dziko mwanu.


Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.


Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.


Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa