Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 22:22 - Buku Lopatulika

22 Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto paguwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Musapereka kwa Chauta nyama zakhungu kapena zopunduka, kapena zoduka chiwalo, kapena zotulutsa mafinya m'thupi, kapena za nthenda zonyerenyesa, kapena zamphere. Nyama zotere asazipereke kwa Chauta, zisakhale nsembe zopsereza pa guwa la Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Musapereke kwa Yehova nyama zakhungu, zovulala kapena zolumala, kapena nyama zimene zikutulutsa mafinya mʼthupi mwake, kapena zimene zili ndi nthenda yonyerenyetsa, kapena zimene zili ndi mphere. Nyama zotere musaziyike pa guwa kuti zikhale nsembe yopsereza kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:22
9 Mawu Ofanana  

Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.


Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.


Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa