Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 22:13 - Buku Lopatulika

13 Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma mwana wamkazi wa wansembeyo akakhala wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya bambo wake monga pa nthaŵi ya utsikana wake, angathe kudyako chakudya cha bambo wake. Koma wapadera asadyeko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:13
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.


Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;


Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.


Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.


Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.


Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.


Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.


Ndipo atatuluka m'nyumba mwake, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina.


Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa