Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 21:9 - Buku Lopatulika

9 Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo mwana wamkazi wa wansembe aliyense akadziipitsa pokhala wachiwerewere, amaipitsa bambo wake. Mwanayo ayenera kumtentha pa moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 21:9
16 Mawu Ofanana  

Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.


Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.


Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?


iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.


Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi.


Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu.


Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.


pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.


ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.


Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali nacho choperekedwacho adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo chifukwa analakwira chipangano cha Yehova, ndi chifukwa anachita chopusa mu Israele.


Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.


Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.


Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa