Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 21:8 - Buku Lopatulika

8 Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa Ine Chauta amene ndimakuyeretsani, ndine woyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 21:8
18 Mawu Ofanana  

Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.


Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,


Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.


Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.


ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.


Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.


kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa