Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 21:5 - Buku Lopatulika

5 Asamete tsitsi la pamutu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ansembe asamete tsitsi kumutu kwao, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zao, kapenanso kudzichekacheka pa thupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “ ‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 21:5
12 Mawu Ofanana  

Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;


Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.


Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.


Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wake, asadzidetse, ndi kudziipsa.


Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.


Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende.


Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pamaso chifukwa cha akufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa