Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 21:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta adauza Mose kuti, “Ulankhule ndi ansembe, ana a Aroni, ndipo uŵauze kuti: Pasapezeke ndi mmodzi yemwe amene adziipitse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 21:1
12 Mawu Ofanana  

Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova.


Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.


Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.


Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.


Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;


Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;


Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa