Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 20:7 - Buku Lopatulika

7 Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nchifukwa chake mudziyeretse, ndipo mukhale oyera, poti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “ ‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 20:7
15 Mawu Ofanana  

Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.


Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.


Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.


Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.


koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;


Pakuti Mulungu sanaitane ife titsate chidetso, koma chiyeretso.


Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simungathe inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu.


Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa