Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 20:5 - Buku Lopatulika

5 pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ineyo ndidzamfulatira munthu ameneyo ndi banja lake lonse. Ndidzaŵachotsa pakati pa anthu anzao, pamodzi ndi onse amene amaŵatsanzira nadziipitsa pakupembedza Moleki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 20:5
13 Mawu Ofanana  

Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.


Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.


ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.


Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.


Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zake kwa Moleki, kuti asamuphe;


Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa