Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 19:8 - Buku Lopatulika

8 koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Munthu aliyense amene aidye, adzasenza tchimo lake chifukwa chakuti waipitsa chinthu choyera cha Chauta. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Munthu aliyense amene adya chakudyacho adzasenza machimo ake chifukwa wayipitsa chinthu chimene ndi choyera kwa Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 19:8
7 Mawu Ofanana  

Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Akakadya konse tsiku lachitatu kali chonyansa, kosavomerezeka:


Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.


Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova;


Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;


Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa