Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 19:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, Mulungu wanu, muchite mwa njira yoti mulandiridwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “ ‘Pamene mukupereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, muyipereke mwanjira yoti ilandiridwe.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 19:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Yehova.


Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.


Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata.


Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto.


kuti mulandiridwe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema, ya ng'ombe, kapena nkhosa kapena mbuzi.


Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.


Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.


Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.


Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m'mawa adye chotsalirapo;


Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa