Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 18:6 - Buku Lopatulika

6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Munthu wina aliyense mwa inu asagone ndi wachibale wake. Ine ndine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “ ‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 18:6
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.


Anavula umaliseche wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anachepsa wodetsedwa ndi kooloka kwake.


Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.


Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.


koma chifukwa cha abale ake enieni ndiwo, mai wake, ndi atate wake, ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi, ndi mbale wake;


koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa