Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 18:5 - Buku Lopatulika

5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nchifukwa chake muchite zimene ndikukulamulani ndipo muzimvera malamulo anga, motero mudzakhala ndi moyo. Ine ndine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 18:5
19 Mawu Ofanana  

ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.


Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA:


Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kuchita chokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.


Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.


Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.


Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.


Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.


Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa.


koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.


kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.


Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa