Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 17:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo paguwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo wansembe awaze magazi ake pa guwa la Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Atatero atenthe mafuta ake, kuti atulutse fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Wansembe awaze magazi ake pa guwa la Yehova limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo atenthe mafuta ake kuti atulutse fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 17:6
12 Mawu Ofanana  

Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.


Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;


kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.


Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.


naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.


Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa