Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 16:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Aroni apereke ng'ombe yamphongoyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini, ndipo motero achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake. Tsono aphe ng'ombeyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 16:11
6 Mawu Ofanana  

Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo achite chotetezera malo opatulikatu, natetezere chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo.


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova analamula.


amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa