Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 14:41 - Buku Lopatulika

41 napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mzinda dothi adapalako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Pambuyo pake wansembe auze anthu kuti apale makoma onse m'kati mwa nyumbayo, ndipo dothi akupalalo akalitaye ku dzala kunja kwa mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 14:41
10 Mawu Ofanana  

amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;


Ndipo adzagumula malinga a Tiro, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.


pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mzinda;


natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.


Ndipo apasule nyumbayo, miyala yake, ndi mitengo yake, ndi dothi lake lonse kumzinda kuzitaya ku malo akuda.


nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.


Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu panjira imeneyo.


a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa