Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 14:32 - Buku Lopatulika

32 Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Limeneli ndilo lamulo la munthu wakhate amene alibe zinthu zoperekera kuyeretsedwa kwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 14:32
12 Mawu Ofanana  

Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;


Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


Chilamulo cha wakhate tsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe;


Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;


limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa