Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 13:57 - Buku Lopatulika

57 ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

57 ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

57 Bangalo likaonekanso pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Zonse zanguwizo muzitenthe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

57 Koma ngati nguwiyo iwonekanso pa chovala chathonje kapena chaubweya ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Chilichonse chimene chili ndi nguwi chiyenera kutenthedwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:57
10 Mawu Ofanana  

Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?


ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;


Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa chovala, kapena chikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;


Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera.


Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa