Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 13:52 - Buku Lopatulika

52 Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Tsono wansembe achitenthe chovalacho, chifukwa nguwiyo yaipitsa chovala chaubweya kapena chathonjecho, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, poti imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chinthucho achitenthe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Wansembe atenthe chovala chathonje kapena chaubweya chija, ngakhalenso chinthu chachikopa chija popeza nguwiyo yachidetsa. Nguwiyo ndi yoopsa choncho chinthucho achitenthe.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:52
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.


Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m'chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m'mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe.


Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.


Ndiponso ngati nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya, kapena chathonje;


ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;


naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.


Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa