Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 13:51 - Buku Lopatulika

51 naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri aiwonetsetsenso nguwiyo. Ikakhala itafalikira pa chovalacho, kapena pa chikopa cha ntchito ya mtundu uliwonse, imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chovalacho ndi choipitsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:51
5 Mawu Ofanana  

ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;


ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse chija cha nthenda masiku asanu ndi awiri;


Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.


ndipo wansembe abwerenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;


pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa