Levitiko 13:3 - Buku Lopatulika3 ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbuu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Wansembe aonetsetse pakhungu pali nthendapo. Akapeza kuti ubweya wa pamalo pali nthendapo wasanduka woyera, ndipo kuti nthendayo yazama ndithu kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe atamuwonetsetsa ndithu, amutchule kuti ndi woipitsidwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa. Onani mutuwo |