Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 13:25 - Buku Lopatulika

25 pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 wansembe aliwonetsetse. Ubweya wapabangapo ukasanduka woyera, ndipo balalo likaoneka kuti lazama, limenelo ndi khate lomwe laphulika pa balalo. Wansembe atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:25
7 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.


Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.


Kapena pamene thupi lidapsa ndi moto pakhungu pake, ndipo mnofu wofiira wakupsawo usanduka chikanga chotuuluka, kapena chotuwa;


Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m'chikangamo, ndipo sichikumba kubzola khungu, koma chazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;


Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;


Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa