Levitiko 13:20 - Buku Lopatulika20 ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'chilondamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'chilondamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Wansembe aonetsetse bwino, ndipo chithupsacho chikazama, ubweya wake nusanduka woyera, wansembeyo amutchule munthu wodwala uja kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yaphulika pachithupsapo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Wansembe aonetsetse bwino ndipo ngati chikuoneka kuti chazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka woyera, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yatuluka mʼchithupsacho. Onani mutuwo |