Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 12:8 - Buku Lopatulika

8 Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma ngati alibe mwanawankhosa, atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, imodzi ikhale ya nsembe yopsereza, ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera, ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 12:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.


ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;


ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;


ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.


Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa