Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 12:7 - Buku Lopatulika

7 ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Wansembeyo apereke zimenezo pamaso pa Chauta potsata mwambo wopepesera mkaziyo. Apo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku matenda ake. Limeneli ndi lamulo la mkazi amene abala mwana wamwamuna kapena wamkazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake. “ ‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 12:7
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;


Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.


ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake.


Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.


pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;


kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.


Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa