Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 12:5 - Buku Lopatulika

5 Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma akabala mwana wamkazi, adzakhala woipitsidwa masabata aŵiri monga pa nthaŵi yake yakusamba. Ndipo mkaziyo adikirebe masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 12:5
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.


Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake.


Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa