Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 11:2 - Buku Lopatulika

2 Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi:

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 11:2
22 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.


Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,


inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.


Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;


Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kutumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:


Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake;


Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.


Chakudya chilichonse chokhala m'mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m'chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa.


Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.


Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.


si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.


Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa