Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 11:11 - Buku Lopatulika

11 inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Zimenezo zikhale zonyansa kwa inu, ndipo musadye. Zikafa zikhalebe zonyansa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 11:11
8 Mawu Ofanana  

Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.


Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo padziko lonse lapansi.


Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa;


Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa.


Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;


Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.


kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.


Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa