Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 10:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mose adauza Aroni ndi ana ake otsalira aja, Eleazara ndi Itamara, kuti, “Tengani zopereka za zakudya zimene zatsalako pa nsembe yotentha pa moto ija, yopereka kwa Chauta, ndipo muzidye zosafufumitsa pafupi pa guwa, pakuti zimenezi nzopatulika kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 10:12
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.


Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.


Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.


Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.


ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero.


Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.


Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.


Ndipo maina ao a ana aamuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa