Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 7:15 - Buku Lopatulika

15 Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ngakhale ndimaŵalera ndi kuŵalimbitsa, komabe amandichita zachiwembu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa, koma amandikonzera chiwembu.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 7:15
18 Mawu Ofanana  

Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.


Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale.


Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.


amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo.


Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake?


Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?


Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;


Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.


Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.


amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu?


chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.


ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;


ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa