Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 5:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndidzalumphira Aefuremu ngati mkango, ndidzambwandira Ayuda ngati msona wa mkango. Ine mwini ndidzaŵakadzula nkuchokapo. Pamene ndizidzaŵaguza, palibe wina aliyense wotha kudzaŵalanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu. Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda. Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo; ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 5:14
16 Mawu Ofanana  

Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango; mubweranso ndi kudzionetsera modabwitsa kwa ine.


chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa.


Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.


Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira.


Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine.


Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa