Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 2:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo ndidzampatsa minda yake yamphesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Kumeneko ndidzambwezera minda yake yamphesa. Ndidzasandutsa Chigwa cha Mavuto kuti chikhale chipata cha kuchiyembekezo. Ndipo kumeneko azidzandiyankha monga m'mene ankandiyankhira pa ubwana wake, atatuluka ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa, ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo. Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake, monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:15
33 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.


Pamenepo anavomereza mau ake; anaimbira chomlemekeza.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi chigwa cha Akori chidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.


Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,


Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?


Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m'dziko muno.


Ndili nacho chiyembekezo popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu.


Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukire masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, womvimvinizika m'mwazi wako.


Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.


Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.


Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.


Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.


Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.


Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.


Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.


Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.


Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.


Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mizinda ya mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.


Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.


Pamenepo Israele anaimba nyimbo iyi, Tumphuka chitsime iwe; muchithirire mang'ombe;


Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.


Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.


Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa