Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 14:7 - Buku Lopatulika

7 Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Aisraele adzapezanso chitetezo mwa Ine. Adzakolola tirigu wambiri, adzachuluka ngati mphesa. Adzakhala otchuka ngati vinyo wa ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake. Iye adzakula bwino ngati tirigu. Adzachita maluwa ngati mphesa ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 14:7
17 Mawu Ofanana  

Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.


Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.


Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.


paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.


Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzavomereza, ati Yehova, ndidzavomereza thambo, ndi ilo lidzavomereza dziko lapansi;


ndi dziko lapansi lidzavomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzavomereza Yezireele.


Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.


Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa