Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 12:10 - Buku Lopatulika

10 Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi padzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndidalankhula ndi aneneri. Ndine amene ndidaŵaonetsa zinthu zambiri ngati kutulo. Ndidalankhula m'mafanizo kudzera mwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndinayankhula ndi aneneri, ndinawaonetsa masomphenya ambiri, ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 12:10
29 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.


Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.


Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;


Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe,


Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvere, simunatchere khutu lanu kuti mumve;


Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;


Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele,


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.


Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.


Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;


Mukhale m'misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m'dziko la Israele akhale m'misasa;


Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;


Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.


Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa