Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hagai 2:12 - Buku Lopatulika

12 Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo ukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezinso zidzasanduka zopatulika? Ansembewo adayankha kuti, ‘Iyai.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ” Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”

Onani mutuwo Koperani




Hagai 2:12
8 Mawu Ofanana  

Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.


Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.


Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.


Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.


Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?


Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu paguwa la nsembe lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa