Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hagai 1:8 - Buku Lopatulika

8 Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kwerani ku mapiri, mukadule nsichi, mudzandimangire Nyumba yoyenera, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiriramo ulemerero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Hagai 1:8
21 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.


Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.


Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


ndi mipambo itatu ya miyala yaikulu, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndalama zochokera kunyumba ya mfumu.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.


Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.


kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mawere a zitonthozo zake; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wake.


Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.


ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.


Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa