Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hagai 1:10 - Buku Lopatulika

10 M'mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 M'mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nkuwonatu mvula yati zii, nthaka yati gwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Choncho, chifukwa cha inu, mitambo yaleka kugwetsa mvula ndipo dziko lapansi laleka kutulutsa zomera.

Onani mutuwo Koperani




Hagai 1:10
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;


Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m'nyengo yake, ndi vinyo wanga m'nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake.


Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;


Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa