Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 50:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Atamwalira bambo wao uja, abale ake a Yosefe adati, “Nanga tidzatani ife, Yosefe akadzayamba kudana nafe ndi kufuna kubwezera zoipa zonse zimene tidamuchita zija?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 50:15
13 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.


Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.


Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu.


Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Ejipito, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake.


Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,


Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.


Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.


popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa