Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 46:32 - Buku Lopatulika

32 ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Anthu ameneŵa ndi abusa, amaŵeta zoŵeta. Nkhosa zao ndi ng'ombe zomwe abwera nazo, pamodzi ndi zinthu zao zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:32
17 Mawu Ofanana  

ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona mu Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani.


Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.


Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.


Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;


Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m'dziko la Kanani, afika kwa ine;


Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani?


Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.


Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.


Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wampesa:


Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.


Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.


Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa