Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 46:26 - Buku Lopatulika

26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Chiŵerengero chonse cha anthu ochokera mwa Yakobe, amene adapita ku Ejipito, chinali 66, osaŵerengera akazi a ana ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:26
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.


Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;


Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:


Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito.


Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.


Makolo anu anatsikira ku Ejipito ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano muchuluke ngati nyenyezi za kumwamba.


Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa