Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 46:15 - Buku Lopatulika

15 Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 (Ana ameneŵa ndiwo amene Leya adabalira Yakobe ku Mesopotamiya kuja, ndipo panalinso mwana wake wamkazi Dina. Adzukulu obadwa mwa Leya analipo 33 onse pamodzi.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:15
14 Mawu Ofanana  

ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.


ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndi ana aamuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele.


Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.


Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa