Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 44:31 - Buku Lopatulika

31 kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 akakangoona kuti iyeyu palibe, basitu akafa. Ndiye kuti ifeyo ndi amene tidzachititse bambo wathu chisoni chofa nacho mu ukalamba wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 ndipo akakaona kuti mnyamatayu palibe, basi akafa. Ife tidzakhala ngati takankhira abambo athu ku manda ndi chisoni.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 44:31
8 Mawu Ofanana  

Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


ndipo ngati mukandichotsera ameneyonso, ndipo ngati chimgwera choipa, mudzanditsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa