Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 44:30 - Buku Lopatulika

30 Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Yuda adapitiriza kulankhula nati, “Nchifukwa chake tsopano ndikabwerera kwathu kwa bambo wanga, mtumiki wanu, opanda mnyamata ameneyu, amene moyo wa bambo wanga uli pa iye,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Tsono ngati tizibwerera kwa mtumiki wanu, abambo athu popanda mnyamatayu, amene moyo wa abambo ake uli pa iyeyu,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 44:30
8 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.


Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.


Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa.


kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.


Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga.


Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!


Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.


Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa