Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 36:24 - Buku Lopatulika

24 Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ana a Zibiyoni ndi aŵa: Aya ndi Ana. (Ameneyu ndiye Ana amene adapeza akasupe otentha m'chipululu, pamene ankadyetsa abulu a Zibiyoni bambo wake.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 36:24
12 Mawu Ofanana  

Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi;


Ana a Sobala ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebala, Sefo ndi Onamu.


Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.


Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana aamuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa.


Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira.


Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.


ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.


Barelenso ndi udzu wa akavalo ndi ngamira anabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira.


ndi woyang'anira ng'ombe zakudya mu Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safati mwana wa Adilai;


Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.


Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru, ngamira, ndi abulu, ndi nyama zonse zokhala m'misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo.


(Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa